The Very Best - Julia Lyrics

Lyrics Julia - The Very Best



Anandipatsa chikondi chosowa
Mwana mkazi ine chim'tima kuda bii
Monga wakhungu kulephera kupenya
Ine uchitsilu chim'chenga m'maso waa
Ndinapusa ndi mtima wanga
Ouma monga mwala ine kupwalala
Pozindikira linali tsiku
Ankanka kwao kumangoni ine nkhawa bii
Julia, Julia usatelo
Julia, Julia bwerera
Julia, Julia usatelo
Julia, Julia bwerera
Ndikagona ndimangolota kuti mwina iye adzabweranso
Nthawi zambiri ndikakhala
Ndimalira kunong'oneza bondo
Ndikanadziwa nkanamupatsa chikondi changa chonse
Ndi mtima wanga wonse
Nkanamupatsa moyo wanga
Bwezi ndithu mpaka lero tikadali limodzi
Julia, Julia usatelo
Julia, Julia bwerera
Julia, Julia usatelo
Julia, Julia bwerera
Ambirife tikapeza chikondi timatayilira
Timayiwalanso
Kuti n'cham'tengo wapatali
Ukapeza chikondi n'chofunika kuchisamalira
Poti monga dzira
Sichichedwa kusweka
Julia, Julia usatelo
Julia, Julia bwerera
Julia, Julia usatelo
Julia, Julia bwerera



Writer(s): Johan Karlberg, Kane Robinson, Etienne Tron De Bouchony De Berard De, Esau Mwamwaya


The Very Best - Warm Heart of Africa
Album Warm Heart of Africa
date of release
14-09-2009




Attention! Feel free to leave feedback.